Mzimu Woyera wa mvula yoyamba udapatsidwa kwa iwo omwe adalandira Mulungu amene adabwera m’thupi mu nthawi ya Mwana. Momwemonso, Mzimu Woyera wamvula yotsiriza umaperekedwa kwa iwo omwe analandira Mulungu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, omwe abwera kuthupi mu nthawi ino ya Mzimu Woyera, ndi omwe adalandira thupi ndi mwazi wa Mulungu kudzera mu pasika ya Pangano Latsopano.
Pamene Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, adadzitcha “ife” Mulungu adatiphunzitsa kudzera mu ubale wapakati pa mthunzi ndi zenizeni zake, kuti tili ndi banja Kumwamba monga tili ndi banja pano padziko lapansi. Kwa ana omwe adazindikira chipulumutso cha Mulungu Atate ndi Mulungu Amayi, Mulungu adaperekanso ntchito yodalitsika yopulumutsa dziko lapansi ndi Mzimu Woyera womwe adawapatsa.
Ndipo anati Mulungu, “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu . . .’’ Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
Genesis1:26–27
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi