Aisrayeli anaiwala mawu a Mulungu amene anawapulumutsa pamene analumidwa ndi njoka zaululu.
M’malomwake, iwo analambira njoka yamkuwayo kwa zaka zoposa 800, koma Hezekiya anathyola njoka yamkuwayo.
Monga chonchi, chinthu chofunika kwambiri ndi mwazi wamtengo wapatali wa Yesu Khristu umene umapulumutsa anthu.
Choncho, tiyenera kuzindikira kuti ngati tiika mtanda, umene uli chida chokha chophera, tidzakhala otembereredwa.
Mtanda unaperekedwa ku Roma kuyambira m’nthaŵi ya Babulo wakale.
Unalowetsedwa mu mpingo cha m’ma AD 431, Yesu atakwera kumwamba ndipo atumwi onse anachoka.
Malinga ndi ziphunzitso za Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, amene anati, “Musalambire mafano,” Mpingo wa Mulungu sumaimika ndi kulambira mtanda kapena mafano alionse.
Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, . . . Usazipembedzere izo, usazitumikire izo;
Eksodo 20:4-5
Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m’malo a m’tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen .
Deuteronomo 27:15
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi