Masiku ano, anthu ambiri padziko lonse
amalambira Mulungu Sande.
Koma tsiku limene Mulungu amatidalitsa ndi
kutilamula kuti tizilikumbukira poliyeretsa ndi
tsiku la Sabata (Loweruka).
Ufumu wakumwamba si malo amene anthu
angapite chifukwa chongokhulupirira kuti kuli
Mulungu komanso kupita kutchalitchi. Ndi okhawo
amene amasunga tsiku la Sabata lomwe ndi
chizindikiro chimene Mulungu anapereka kwa
anthu ake ndi amene angathe kupita
ku ufumu wakumwamba.
Monga momwe anthu amphamvu ogonjetsa
otchuka, andale, ndi anthu olemera anafera,
anthu onse amafa ndi kukhala kwamuyaya
kaya kumwamba kapena mu Malawi amoto.
Pamene tazindikira zimenezi, tiyenera kutsatira
njira ya ku ufumu wakumwamba imene
Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi
amatiphunzitsa, ndilo, tsiku la Sabata m’Baibulo.
Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale
lopatulika. Masiku asanu ndi limodzi
uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako
zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri
ndilo Sabata la Yehova Mulungu
wako;...chifukwa chake Yehova
anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.
Eksodo 20:8-11
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye,
Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa
Kumwamba; koma wakuchitayo
chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.
Mateyu 7:21
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi