Esau ndi Yudasi Isikarioti anataya madalitso chifukwa cha mawu osasamala omwe analankhula, ndipo wachifwamba wa kumanja ndi anzake atatu a Danieli analandira madalitso ochuluka kuchokera kwa Mulungu chifukwa cha mawu amene analankhula ndi chikhulupiriro.
Popeza kuti mawu otuluka m’kamwa mwathu satha koma amabwerera kwa ife pa Tsiku la Chiweruzo, nthawi zonse Mulungu amatiphunzitsa kuganiza kambirimbiri tisanalankhule komanso kuti tikhale odekha pokwiya.
Tikazindikira kuti tinagwetsedwa kuchokera kumwamba chifukwa chochimwa, sitidzakhumudwa ndi chilichonse. M'malo mwake, titha kukhala ndi moyo wodalitsika pokhala othokoza ndi kunena zinthu zabwino potsatira ziphunzitso za Mulungu chifukwa choti titha kukhala ndi Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi omwe abwera mu m'badwo wa Mzimu Woyera.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.... Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.... adzakhala wodala m'kuchita kwake.
Yakobo 1:19-25
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi