Tikumana ndi mayesero, masautso, ndi kulemedwa kwakukulu kwa mtanda panjira yathu yachikhulupiriro, iwo amene amaona zovutazi ngati masautso, kuganiza, “Ndine watsoka,” adzakhaladi osasangalala, koma amene amazindikira madalitso ndi kupereka mayamiko m’nyengo zimenezi adzapeza chisangalalo ndi kulowa mu ufumu wakumwamba.
Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi amati, “Kondwerani nthawi zonse ndipo yamikani m’nyengo zonse,” ndipo amatiphunzitsa kukhala ndi moyo wokhutitsidwa chifukwa umbombo wa dziko umabweretsa mayesero ndi kusasangalala.
Iwo amatiphunzitsa kudzizoloweretsa tokha kukhala aumulungu pakusintha nyengo iliyonse yosakhala bwino kukhala mphamvu ya chimwemwe.
Kondwerani nthawi zonse;pempherani kosaleka;m'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
1 Atesalonika 5:16-18
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye. Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.
Yakobo 1:12-15
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi