Magome oyamba a Malamulo Khumi anaphwanyidwa pamene Aisraeli analambira mwana wa ng’ombe wagolide. Komabe, Mulungu adapereka gawo lachiwiri la Malamulo Khumi pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri. Mulungu adasankha tsiku lino ngati Tsiku Lachitetezero lomwe lili ndi lonjezo lakukhululukidwa kwa machimo, ndipo adasankha tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri ngati Phwando la Malipenga.
Mtumwi Yohane adati mapemphero onse amakhala utsi wa zofukiza ndikupita pamaso pa Mulungu.
Tiyenera kuzindikira kuti Mzimu Woyera Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi akutetezera anthu omwe ali ofooka, omwe amatsata zinthu zopanda pake, ndipo amalephera kuwona madalitso osatha Kumwamba. Tiyenera kusunga Maphwando a Mulungu ndi mitima yolapa, ndikupereka mayamiko chifukwa cha chisomo chawo.
‘Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro. Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu. Pakuti chimene tizipempha monga chiyenera sitidziwa, koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka.’
Aroma 8:25–26
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi