Ophunzira, amene anaona Yesu akukwera kuchokera
ku Phiri la Azitona, anazindikira kuti popanda
kuvala mzimu woyera wa Mulungu, Uthenga
Wabwino sungalalikidwe padziko lonse lapansi.
Chotero, iwo anapemphera mowona mtima kwa
masiku khumi kuchokera pa Tsiku la Kukwera
Kumwamba kufikira pa Tsiku la Pentekoste,
kupempha Mzimu Woyera wa mvula yoyambayo.
Pamene Eliya anagonjetsa aneneri
onyenga 850 pa Phiri la Karimeli,
pemphero linatsogolera chipambanocho.
Yesu, Khristu Ahnsahnghong, ndi Mulungu Amayi,
amene anabwera padziko lino lapansi kudzapulumutsa
anthu, anapereka chitsanzo poyamba ntchito
Yawo ya uthenga wabwino ndi mapemphero
a m’bandakucha tsiku lililonse.
Choncho, mamembala a Mpingo wa
Mulungu, nawonso, amayamba tsiku
lawo, kupeza mphamvu zauzimu
kudzera mu pemphero.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa
inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani,
ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Pakuti yense wakupempha alandira;
ndi wofunayo apeza; ndi iye
amene agogoda adzamtsegulira.
Mateyu 7:7-8
Chifukwa chake ndinena ndi inu,
Zinthu zilizonse mukazipemphera
ndi kuzipempha, khulupirirani kuti
mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
Marko 11:24
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi