Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu
Amayi anabwera ku dziko lino
lapansi mu thupi ndipo
anayenda njira ya zowawa
chifukwa cha chipulumutso
cha ana awo amene akukhala
mu zowawa chifukwa cha machimo
amene anachita kumwamba.
Tikazindikira chikondi ndi nsembe
ya Makolo athu auzimu ndi
kudzitamandira pa Iwo, Mulungu
adzativomereza ife monga
“ana Anga” pamaso pa angelo
ndi kutipatsa madalitso.
Anthu a Mulungu anadzitamandira
ponena za Yehova Mulungu
m’badwo wa Atate
ndi Yesu m’badwo wa Mwana.
Momwemonso, tiyenera kudzitamandira
za Khristu Ahnsahnghong ndi
Mulungu Amayi, amene anabwera
ngati Mzimu ndi Mkwatibwi
mu m'badwo wa Mzimu Woyera.
Tiyeneranso kuzindikira mbava zauzimu
zomwe zimabera mitima yathu,
kutembenuzira mitima yathu kwa
Mulungu, ndi kuwononga miyoyo yathu.
Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense
akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde,
Mwana wa Munthu adzamvomereza
iye pamaso pa angelo a Mulungu;
Koma iye wondikana
Ine pamaso pa anthu, iye
adzakanidwa pamaso
pa angelo a Mulungu.
Luka 12:8-9
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi