Zochita za munthu aliyense, zomwe zalembedwa m’Buku la Moyo, sizifafanizidwa ngakhale patapita zaka zikwizikwi, koma Mulungu amaziweruza ngati zili zoyenera kulandira mphoto kapena chilango. Moyenerana, adzatenga nawo mbali mu kuuka kwa olungama, kumene kudzawatsogolera kupita Kumwamba, kapena kuuka kwa oipa kumene kudzawatsogolera ku gehena.
Oyera mtima a Mpingo woyamba anawona kuuka kwa Yesu ndipo adakhazikika m’chikhulupiriro chawo. Masiku ano, Khristu Ahnsahnghong ndi Amayi Akumwamba amatiphunzitsa kukhala ndi chikhulupiriro mu kuuka ndi kusandulika. Amaphunzitsa kuti anthu onse akamaopa Mulungu ndi kulapa kotheratu machimo awo, adzasandulika kukhala thupi lauzimu ndi kubwerera ku dziko la angelo.
“Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama. M’menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.”
Machitidwe 24:15–16
Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu; . . . asanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero.
Afilipi 3:20–21
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi