Monga momwe chingwe chowongolera chimaikidwa kuti chiwone ngati nyumba ikumangidwa mowongoka kapena ayi, Mulungu akupereka ziyeso kwa ana Ake kuti awone ngati akumanga nyumba ya chikhulupiriro chawo mowongoka monga momwe Mulungu anachitira kwa Yobu, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Komabe, madalitso Ake amatsatira nthawi zonse pamapeto.
Christ Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi aphunzitsa mamembala amene akumanga nyumba za chikhulupiriro chawo lero kuti Mulungu akamayesa dziko lonse lapansi, Iye adzasanthula zolankhula za munthu aliyense, zochita zake, ndi mitima yake ndiyeno kubweretsa tsoka kwa osakhulupirira amene amang’ung’udza ndi kudandaula. Iwo aphunzitsanso mamembala kuti nthawi zonse aziganizira za Kumwamba ndi Mulungu yekha posatengera zomwe zikuchitika.
Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m’dzanja lake. . . . Nati Ambuye, “Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso.”
Amosi 7:7–8
“Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.”
Chivumbulutso 2:23
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi