Anthu ambiri amakhulupirira
kuti kungopita kutchalitchi,
amakhala anthu oona a Mulungu.
Komabe, ndi lamulo la Mulungu
la moyo, amasiyanitsa pakati
pa anthu oona ndi abodza.
Anthu oona a Mulungu, okhala ndi
unzika wakumwamba, ayenera kusunga
tsiku la Sabata, lokumbukira mphamvu
ya Mlengi, ndi Paska,
yokumbukira mphamvu ya Momboli.
Monga mmene Solomoni, mfumu yanzeru,
anagwiritsira ntchito njuchi ndi agulugufe kuti
asiyanitse duwa lenileni ndi duwa lochita
kupanga, Mulungu amasiyanitsa anthu ake oona
kudzera m’malamulo ake monga tsiku la Sabata ndi Paska.
Masiku ano, anthu ambiri padziko lonse lapansi
amasunga malamulo a Mulungu—chizindikiro
cha anthu a Mulungu—obwezeretsedwa
kudzera mu ziphunzitso za Khristu
Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi.
Pakuti ambiri amayenda, za amene
ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo
tsopanonso ndikuuzani ndi kulira,
ali adani a mtanda wa Khristu;
chitsiriziro chao ndicho kuonongeka,
mulungu wao ndiyo mimba yao,
ulemerero wao uli m'manyazi ao,
amene alingirira za padziko.
Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; . . .
Afilipi 3:18-20
Ndipo muzisunga Sabata ; popeza ndilo
lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa
aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira
ntchito m'mwemo, munthu ameneyo
achotsedwe mwa anthu a mtundu wake.
Eksodo 31:14
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi