Sitiyenera kukhala ngati Mfumu Saulo yemwe adamasulira mawu a Mulungu momwe adafunira ndikuwamvera pang’ono. M’malo mwake, tiyenera kusunga Pasika ngati Mfumu Hezekiya, kutembenuza mitima yathu yolowerera kuchoka kudziko ndikubwerera kwa Mulungu kudzera muzakhumi ndi zopereka monga zalembedwera m’buku la Malaki. Uku ndiko kulapa.
Tsiku la Chitetezero ndi tsiku lomwe machimo athu onse omwe tidachita Kumwamba ndi machimo omwe tidachita Padziko Lapansi mosadziwa ndi mosazindikira amaperekedwanso kwa satana, yemwe ndiye woyambitsa machimo onse.
Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi adatidziwitsa kuti kulapa kwathunthu kungachitike kudzera pa Madyerero a Pangano Latsopano, omwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu.
“Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” ati Yehova wa makamu. “Koma inu mukuti, ‘Tibwerere motani?’ Kodi munthu adzalanda za Mulungu? . . . Limodzilimodzi la magawo khumi ndi zopereka.”
Malaki 3: 7-8
Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israele lonse . . . kuti abwere kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska ku Yerusalemu. “. . . bwerani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele . . .”
2 Mbiri 30:5–6
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi