M’nthawi ya Mose, Mulungu anapulumutsa Aisiraeli amene anacita Paskha ku mliri ndipo analanga mabanja onse a ku Iguputo amene sanacite Pasika. Izi zikutiwonetsa ife momwe tingapulumutsidwe ku masoka ndi kulandira moyo wosatha mu nthawi inonso.
Paskha wa Pangano Latsopano ndi tsiku limene anthu adzalandira thupi ndi mwazi wa Mulungu ndipo amasindikizidwa ngati ana a Mulungu, ndipo ndi tsiku limene anakhululukidwa machimo awo amene anachita Kumwamba ndi kulandira moyo wosatha.
Ndicho chifukwa chake Mulungu amapereka mwayi winanso wosunga Paskha pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri mwa kalendala yopatulika, akufunitsitsa kuti dziko lonse lapansi lichite Paskha ndi kulandira chipulumutso.
Nena ndi ana a Israele… koma azichitira Yehova Paska. Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa. Asasiyeko kufikira m’mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska. Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
Numeri 9:10–13
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi