Mulungu anapatsa anthu, amene anachimwa kumwamba ndi kuthamangitsidwira ku Dziko Lapansi, mzinda wothawirako, mwayi wolandira chikhululukiro cha machimo ndi kubwerera ku ufumu wakumwamba kudzera m’malamulo Ake.
Kumbali ina, chiweruzo cha Mulungu chidzafika pa iwo amene aswa pangano ndi kulipeputsa.
Ndi chisomo cha Mulungu chokha chomwe anthu, omwe amafa chifukwa cha machimo awo, angapeze moyo wosatha.
Pamene Mulungu amaphunzitsa anthu njira ya moyo mu m’badwo wa Atate, m’badwo wa Mwana, ndi m’badwo wa Mzimu Woyera, iwo amene amabwera ku Ziyoni ndi kusunga Paska wa moyo, kukhulupirira mawu Ake, adzapulumutsidwa, koma iwo amene sakhulupirira mawu Ake ndi kusasunga iwo adzalangidwa pamapeto pake.
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Aroma 6:23
Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu,
ndi chikhulupiriro cha Yesu.
Chivumbulutso 14:12
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi