Anthu amene amakhulupirira Mulungu ayenera kusunga Phwando la Misasa motsatira ziphunzitso za Mulungu. Izi zili choncho chifukwa Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Zekariya kuti adzapereka Mzimu Woyera kwa iwo amene amasunga Phwando la Misasa ndi kubweretsa chilango kwa iwo amene salisunga.
Pa kubwera Kwake koyamba, Yesu anapereka Mzimu Woyera; pa kubwera Kwake kwachiwiri, Mzimu ndi Mkwatibwi amapereka Mzimu Woyera pa Phwando la Misasa. Maulosi a m’Baibulo akuti, “Mzimu ndi Mkwatibwi amapereka madzi amoyo,” “Madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu,” ndi “Mtsinje wa madzi amoyo umatuluka pa mpando wa chifumu wa Mulungu” akuneneratu kuti Amai Akumwamba a ku Yerusalemu adzapereka Mzimu Woyera ndi ziphunzitso zotsogolera ku moyo.
Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira. Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena,... Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake. Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire... Yohane 7:2–39
Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere. Chivumbulutso 22:17
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi