Mulungu anakhazikitsa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wa kalendala yopatulika kukhala Phwando la Malipenga kuti tikumbukire Tsiku la Chitetezero, pokumbukira nthawi imene Iye anakhululukira machimo a Aisrayeli amene anagwa m’kulambira mafano ndi kuwapatsa malamulo khumi achiwiri. Komanso, monga momwe malipenga analizidwira pa Phwando la Malipenga kuitanira ku kulapa, Yesu anabweranso padziko lapansi ndipo analimbikitsa anthu kulapa, ponena kuti, “Lapani.”
Monga tikuonera mu Fanizo la Mwana Woloŵerera komanso mu mbiri ya Yona wotsogolera anthu 120,000 ku Nineve ku chipulumutso, madalitso aakulu ochokera kwa Mulungu amakhala okonzedwa nthawi zonse kutsatira nchito ya kulapa. Leronso, tiyenera kukwaniritsa kulapa kwathunthu—monga Yona—chifukwa cha maso ndi mitima yathu imene tatembenukira ku dziko lapansi, ndipo tiyenera kuliza lipenga, kuitana dziko lonse lapansi kuti libwerere kwa Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amai.
Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.
Chifukwa chake ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israele, yense monga mwa njira zake, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi