Yesu anaphunzitsa anthu kudzera mu Fanizo la Munthu Wolemera ndi Lazaro kuti
moyo padziko lapansi si mapeto. Lazaro, ngakhale kuti anali wosauka padziko lapansi,
anakhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba ndipo m’kupita kwa nthawi anapeza chimwemwe.
Kumbali ina, munthu wolemerayo ankakhala moyo wapamwamba, koma anakhala woyendayenda.
Iye analephera kukonzekera ufumu wakumwamba ndipo pomalizira pake anazunzika mu gehena.
Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi anapatsa anthu umboni wa
makolo akale achikhulupiriro monga Abrahamu ndi Mose amene anati,
“Ife ndife alendo ndi ogonera padziko lapansi pano.”
Kupyolera mu zolembedwa zimenezi za m’Baibulo, Iwo anaunikira anthu
onse kuti kwawo kwenikweni kumene ayenera kubwererako ndiwo ufumu wakumwamba.
Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu
adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
Ahebri 11:13
Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.
M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. . . .
pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. . . . kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
Yohane 14:1–3
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi