Mu m'badwo wa Mzimu Woyera, Mulungu analosera m'Baibulo kuti padzakhala nkhondo yaikulu yauzimu pakati pa Mkaziyo ndi otsala a mbeu Yake ndi Satana ndi otsatira ake. Pamene Mulungu amalekanitsa iwo amene adzapulumutsidwe kwa iwo amene sadzapulumutsidwa, mwakuima kumbali ya Mkazi kokha, amene ndi Mulungu Amai, tingathe kupambana nkhondo yaikulu yauzimu ndi kulandira madalitso a chipulumutso.
Mulungu Ahnsahnghong momveka bwino amatiuza kuti Mulungu Amai alipo kudzera mu dongosolo la banja la padziko lapansi ndi ndondomeko ya kulengedwa kwa Hava komanso mamembala a Mpingo wa Mulungu, otsala mbeuya Mkazi, ayenera kulalikira ulemerero wa Yerusalemu Amai ku dziko lapansi.
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu. Ndipo chinjokacho chinakaimirira m'mbali mwa nyanja. . . . Chivumbulutso 12: 17-13:1
Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete, ndipo musamlole akhale chete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m'dziko lapansi. Yesaya 62:6–7
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi