Monga mmene Adamu ndi Hava
anachimwa chifukwa anaiwala lamulo la
Mulungu lakuti, “Usadye chipatso cha
mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa,”
tikaiwala chilamulo cha Mulungu,
timachita uchimo ndi kubwela zionongeko.
Ngakhale m’nthawi ino, Mulungu akunena
kuti chionongeko chomalizira chidzabwera
chifukwa chakuti dziko laiwala chilamulo cha
Mulungu—tsiku la Sabata ndi Paska wa
pangano latsopano, ndipo sakusunga izo.
Anthu ndi mizimu [angelo] imene
anachimwa kumwamba ndipo
anaponyedwa padziko lapansi pano.
Iwo angabwerere kumwamba kokha
ngati amvera mawu a Mulungu
ali padziko lapansi pano.
Monga momwe Mfumu Hezekiya analandira
madalitso posunga chilamulo [Paska] molingana
ndi mawu a Mulungu, Mpingo wa Mulungu
umamvera chifuniro cha Mulungu posunga
lamulo la Mulungu—pangano latsopano.
Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu
wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi
maweruzo ake, ndi malemba ake,
amene ndikuuzani lero lino;
Deuteronomo 8:11
Si yense wakunena kwa Ine,
Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu
wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro
cha Atate wanga wa Kumwamba.
Ambiri adzati kwa Ine tsiku
lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi
sitinanenere mau m'dzina lanu, . . . ndi
kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?
. . . Sindinakudziweni inu nthawi zonse;
chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
Mateyu 7:21-23
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi