Baibulo mwaulosi limafotokoza m’badwo uno monga nthawi ya mavuto aakulu.
Pamene nkhondo pakati pa mayiko ndi zionongeko zosawerengeka za nyengo
zikuyenda, anthu amapanga mapulani oti athawire mlengalenga,
kuya kunsi kwa nyanja, kapena pansi pa nthaka.
Komabe, Baibulo limanena kuti palibe pothawirapo pachipulumutso
kupatula Ziyoni, kumene Mulungu Amayi amakhala.
Monga Mulungu anaulula ndi kutanthauzira maloto a Mfumu Nebukadinezara kwa
Daniele, lero Iye waulula kuti chitetezo chotetezeka pakati pa zionongeko ndi Mulungu Amayi.
Monga ana amamva kutetezeka kwambiri m’manja mwa amayi awo panthawi
yowopsa, Mulungu waulula kuti Mulungu Amayi ndiye malo otetezeka kwambiri kwa anthu pamavuto.
Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova.
Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja,
ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova. . . .
Zefaniya 1:2–3
Koma kapolo woipa akanena mumtima
mwake, Mbuye wanga wachedwa;
nadzayamba kupanda akapolo anzake,
nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera;
mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku
losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye,
nadzamdula, nadzaika pokhala pake
ndi anthu onyenga; pomwepo
padzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Mateyu 24:48-51
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi