Nowa anakhulupirira madalitso a Mulungu ngakhale kuti anakumana ndi kusungulumwa pamene anamanga chingalawa kwa nthawi yaitali. Mose anakonda kuvutika ndi anthu a Mulungu m’malo mosangalala ndi ulemerero wake monga kalonga ku Ejipito. Mtumwi Paulo anasangalala ndi mwayi wopereka ufumu wakumwamba kwa anthu, ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri. Momwemonso, mamembala a Mpingo wa Mulungu amayenda mosangalala m’njira yachikhulupiriro, atanyamula mitanda yawo.
Amayi akumwamba nthawi zonse amatikumbutsa kuti, “Kodi sitili ndi chiyembekezo cha ufumu wakumwamba?” Chifukwa chake, kaya ndi oyera mtima kapena a zaubusa omwe akugwira ntchito pa nzere woyambirira, aliyense ayenera kuyang’ana madalitso a ufumu wakumwamba wokonzedwa kupitirira zopinga zomwe zikuchitika pamaso pathu pamene tikunyamula mitanda yathu.
nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho. Ahebri 11: 26
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu . . . ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Aroma 8:13-18
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi