Tsiku la zipatso zoyamba mu Chipangano Chakale ndi tsiku la kuuka kwa akufa mu Chipangano Chatsopano. Ndi ulosi umene unayenera kukwaniritsidwa Sunday.
Pa tsiku loyamba la sabata pamene Aisiraeli anatuluka mu Iguputo n’kufika kutsidya lina la Nyanja Yofiira. Mulungu anasankha tsiku limeneli kukhala Tsiku la Zipatso zoyamba, ndipo anachititsa Aisrayeli kulisunga tsiku lotsatira Sabata (Sunday) chaka chilichonse. Yesu anaukitsidwa pa tsiku loyamba la sabata (Sunday), kukwaniritsa ulosi wonena za Tsiku la Zipatso Zoyamba.
Malinga ndi ulosi wa pa Tsiku la Zipatso zoyamba, pamene mtolo wa tirigu unaperekedwa kwa Mulungu, Yesu anaukitsidwa monga zipatso zoyamba za amene anagona ndipo anapereka chiyembekezo cha chiukitsiro kwa anthu onse. Pokhulupirira izi, Mpingo wa Mulungu umakondwerera Tsiku la Kuuka kwa Akufa chaka chilichonse.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, “Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m’dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe; ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.”
Levitiko 23:9–11
Koma tsiku loyamba la sabata, mbandakucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza. Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda. Ndipo m’mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. Ndipo kunali, m’mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira.
Luka 24:1–6
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi