Monga kwalembedwa, “[O]nse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo,” ndipo monga Yesu ananenera, “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, . . . nanyamule mtanda wake . . . nanditsate Ine,” kuvutika kwakanthawi kumatsatira miyoyo ya onse amene amakhala ndi moyo wofuna ulemerero wa ufumu wakumwamba.
Esau ndi Yudasi Isikariyoti anakhala moyo monga mwa thupi, kutsata zosangalatsa za uchimo, ndipo pamapeto pake anataya madalitso a ufumu wa kumwamba. Komabe, Mose, Yakobo, Daniele, ndi anzake atatu anagonjetsa mavuto mwa kuona zosangalatsa za kumwamba kukhala zofunika kwambiri. Momwemonso, mamembala a Mpingo wa Mulungu amaika chiyembekezo chawo mu zosangalatsa za kumwamba zomwe Mulungu adalonjeza, akudzipereka kulalikira madalitso a Tsiku la Sabata la pangano latsopano ndi Paska, monga momwe Iye adalamulira.
Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi; nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho. Ahebri 11:24–26
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi