Pamene ana a Mulungu akhala mchere ndi kuunika kwa dziko lapansi motsatira ziphunzitso za Mulungu, kusonyeza ulemerero wa Mulungu kudzera mu ntchito zawo zabwino, ndikutsogolera anthu kwa Mulungu ndi choonadi cha pangano latsopano, Mulungu adzakondwera ndi kuwapatsa madalitso ochuluka pa tsiku limene adzaima pamaso pake.
Ngati talandira Khristu Ahnsahnghong ndi Yerusalemu Amai Akumwamba mu m’badwo wa Mzimu Woyera, kuyambira tsopano, tiyenera kutaya zizolowezi zoipa zophunzitsidwa kuchokera kudziko lapansi ndi kuvala umunthu watsopano monga Akhristu. Pamene dziko lino likutaya umulungu wake mopitirira muyeso ndipo likukhala mopotozeka ndi moipa, tiyenera kuzindikira kuti tsiku la chiweruzo cha Mulungu lili pafupi, monga momwe zinalili m’masiku a Nowa ndi Loti, ndipo tikhale ndi moyo waumulungu koposa.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro. Aroma 12:1–2
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi